Psalms 2

1Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu?
Akonzekeranji zopanda pake anthu?
2Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo;
ndipo olamulira asonkhana pamodzi
kulimbana ndi Ambuye
ndi wodzozedwa wakeyo.
3Iwo akunena kuti, “Tiyeni timasule magoli awo
ndipo titaye zingwe zawo.”

4Wokhala mmwamba akuseka;
Ambuye akuwanyoza iwowo.
5Ndipo iye awadzudzula mu mkwiyo wake
ndi kuwaopseza mu ukali wake, kunena kuti,
6“Ine ndakhazikitsa mfumu yanga
pa Ziyoni, phiri langa loyera.”
7Ine ndidzalengeza zimene Yehova walamula:

Iye anati kwa Ine, “Iwe ndiwe mwana wanga;
lero Ine ndakhala Atate ako.
8Tandipempha,
ndipo ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu ikhale cholowa chako;
malekezero a dziko lapansi kuti akhale chuma chako.
9Iweyo udzawalamulira ndi ndodo yaufumu yachitsulo;
udzawaphwanya zidutswazidutswa ngati zowumba zadothi.”

10Kotero, inu mafumu, chenjerani;
chenjezedwani, inu olamulira a dziko lapansi.
11Tumikirani Yehova mwa mantha
ndi kukondwerera ulamuliro wake monjenjemera.
12Mpsopsoneni mwanayo kuti angakwiye;
kuti mungawonongedwe mʼnjira zanu,
pakuti ukali wake utha kuuka mʼkanthawi kochepa.
Odala ndi onse amene amathawira kwa Iye.
Copyright information for NyaCCL